Ezekiel 24:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa gulu la nkhosa musankhulepo nkhosa yabwino kwambiri, ndipo muike nkhuni pansi pa mphikawo. Madziwo aŵire, kenaka muphike nyama ija pamodzi ndi mafupa omwe’.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tengako choweta chosankhika, nuikire mafupa mulu wa nkhuni pansi; ubwadamuke, ndi mafupa ake omwe uwaphike m'mwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa gulu la nkhosa musankhepo nkhosa yabwino kwambiri. Muyike nkhuni pansi pa mʼphikawo. Madzi awire. Kenaka muphike nyamayo pamodzi ndi mafupa omwe.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tengako coweta cosankhika, nuikire mafupa mulu wa nkhuni pansi; ubwadamuke, ndi mafupa ace omwe uwaphike m'mwemo.