Ezekiel 24:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa mzinda wamagaziwe, tsoka kwa mphika wa dzimbiri lokangamira ndi losachoka. Mutulutsemo nthuli imodziimodzi, osasankhula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsoka mudzi wokhetsa mwazi, mphika m'mene muli dzimbiri, losauchokera dzimbiri lake; uchotsemo chiwalochiwalo; sanaugwere maere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova akuti, “ ‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi, tsoka kwa mʼphika wadzimbiri; dzimbiri lake losachoka! Mutulutsemo nthuli imodzimodzi osasankhulapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Tsoka mudzi wokhetsa mwazi, mphika m'mene muli dzimbiri, losaucokera dzimbiri lace; ucotsemo ciwalo ciwalo; sanaugwera maere.