Ezekiel 25:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzalanga Edomu ndi dzanja la anthu anga Aisraele. Adzamchita monga m'mene mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzafunire. Choncho adzaona kulipsira kwanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzalibwezera Edomu chilango mwa dzanja la anthu anga Israele; ndipo adzachita m'Edomu monga mwa mkwiyo wanga, ndi ukali wanga; motero adzadziwa kubwezera chilango kwanga, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzalanga Edomu ndi dzanja la anthu anga Aisraeli. Adzalanga anthu a ku Edomu molingana ndi mkwiyo ndi ukali wanga. Choncho adzaona kulipsira kwanga akutero Ambuye Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzalibwezera Edomu cilango mwa dzanja la anthu anga Israyeli; ndipo adzacita m'Edomu monga mwa mkwiyo wanga, ndi ukali wanga; motero adzadziwa kubwezera cilango kwanga, ati Ambuye Yehova.