Ezekiel 25:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵalipsira koopsa ndi kuŵalanga mwaukali kwambiri. Ndikadzaŵalanga choncho, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzawabwezera chilango chachikulu, ndi malango ankharwe; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwabwezera chilango Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawabwezera chilango choopsa ndipo ndidzawalanga mu mkwiyo wanga. Ndikadzawalipsira ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzawabwezera cilango cacikuru, ndi malango ankharwe; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwabwezera cilango Ine.