Ezekiel 25:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Unene kuti, inu Aamoni, imvani mau a Ambuye Chauta akuti, ‘Paja mudatchula mau onyodola, mutaona malo anga opatulika akuipitsidwa, nthaka ya Israele itaguga, ndipo anthu a ku Yuda atatengedwa ukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nunene kwa ana a Amoni, Tamverani mau a Ambuye Yehova, Atero Ambuye Yehova, Popeza unati, Onyo, kunena malo anga opatulika; muja anadetsedwa ndi kunena dziko la Israele; muja linapasuka ndi kunena nyumba ya Yuda; muja adalowa kundende;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awawuze kuti, ‘Inu anthu a ku Amoni, imvani zimene Ambuye Yehova akunena. Iye akuti: Inu munanena mawu onyoza pamene Nyumba yanga yopatulika inkayipitsidwa. Munanyozanso dziko la Israeli pamene linaguga ndiponso anthu a ku Yuda pamene anatengedwa ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nunene kwa ana a Amoni, Tamverani mau a Ambuye Yehova, Atero Ambuye Yehova, Popeza unati, Onyo, kunena malo anga opatulika; muja anadetsedwa ndi kunena dziko la Israyeli; muja linapasuka ndi kunena nyumba ya Yuda; muja adalowa kundende;