Ezekiel 25:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ndidzakuperekani m'manja mwa anthu akuvuma. Adzakhoma mahema ao ndi kumanga nyumba zao m'dziko mwanu. Adzakudyerani zipatso zanu, adzakumwerani mkaka wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake taona, ndidzakupereka kwa ana a kum'mawa ukhale waowao, kuti amange misasa yao mwa iwe, namange pokhala pao mwa iwe, iwo adzadya zipatso zako ndi kumwa mkaka wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Ine ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu akummawa ngati cholowa chawo. Iwo adzamanga misasa yawo ndi kukhoma matenti awo pakati panu. Adzadya zipatso zanu ndi kumwa mkaka wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace taona, ndidzakupereka kwa ana a kum'mawa ukhale wao wao, kuti amange misasa yao mwa iwe, namange pokhala pao mwa iwe, iwo adzadya zipatso zako ndi kumwa mkaka wako.