Ezekiel 25:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzasandutsa Raba kuti akhale busa la ngamira, ndipo ndidzasandutsa mizinda ya Aamoni kuti ikhale makola a nkhosa. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzayesa Raba khola la ngamira, ndi ana a Amoni popumula zoweta zazing'ono; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzasandutsa Raba kuti akhale busa la ngamira ndi mizinda ya Aamoni kuti ikhale makola a nkhosa. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzayesa Raba khola la ngamira, ndi ana a Amoni popumula zoweta zazing'ono; matero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.