Ezekiel 25:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Mudaomba m'manja ndi kulumphalumpha mokondwa, ndipo mudanyodola dziko la Israele ndi kulinyoza ndi mtima wonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Ambuye Yehova, Waomba manja, ndi kuvina, ndi kukondwera ndi chipeputso chonse cha moyo wako, kupeputsa dziko la Israele,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu munawomba mʼmanja ndi kumalumphalumpha. Munkakondwa mu mtima mwanu pamene munkanyoza dziko la Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Ambuye Yehova, Waomba manja, ndi kubvina, ndi kukondwera ndi cipeputso conse ca moyo wako, kupeputsa dziko la Israyeli,