Ezekiel 25:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ine ndidzakukanthani ndi dzanja langa ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha mitundu ina ya anthu. Ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ina ya anthu, ndipo ndidzakufafanizani pa dziko lapansi. Ndidzakuwonongeranitu, ndipo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake taona, ndakutambasulira dzanja langa, ndipo ndidzakupereka ukhale chofunkha cha amitundu, ndi kukudula mwa mitundu ya anthu, ndi kukutayikitsa m'maiko, ndidzakuononga; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake ndidzatambasula dzanja langa kuti ndikulangeni, ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha anthu a mitundu ina. Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukufafanizani mʼmayiko onse. Ndidzakuwonongani, ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova!’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cikufwa cace taona, ndakutambasulira dzanja langa, ndipo ndidzakupereka ukhale cofunkha ca amitundu, ndi kukudula mwa mitundu ya anthu, ndi kukutayikitsa m'maiko, ndidzakuononga; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.