Ezekiel 26:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akavalo ake ochuluka adzakukwirira ndi fumbi lao. Malinga ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo ndiponso ndi mkokomo wa mikombero ya magaleta poloŵa pa zipata zako, monga momwe zimachitikira poloŵa mu mzinda umene wagumulidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza achuluka akavalo ake, fumbi lao lidzakukuta; malinga ako adzagwedezeka ndi phokoso la apakavalo, ndi njinga za magaleta, polowa iye pa zipata zako, monga umo amalowera m'mudzi popasukira linga lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akavalo ake adzakhala ochuluka kwambiri kotero kuti adzakukwirira ndi fumbi lawo. Makoma ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo, ngolo ndi magaleta pamene iye adzalowa pa zipata monga mmene amalowera mu mzinda umene makoma ake agwetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Papeza acuruka akavalo ace, pfumbi lao lidzakukuta; malinga ako adzagwedezeka ndi phokoso la apakavalo, ndi njinga za magareta, palowa iye pa zipata zako, monga umo amalowera m'mudzi popasukira linga lace.