Ezekiel 26:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzafunkha chuma chako ndi kulanda malonda ako. Malinga ako adzaŵagumula, ndipo nyumba zako zokongola adzazigwetsa. Miyala yako, mitengo yako ndi dothi lako lomwe adzaziponya m'nyanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzalanda chuma chako ndi kufunkha malonda ako, nadzagwetsa malinga ako ndi kupasula nyumba zako zofunika, nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi fumbi lako, m'madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzafunkha chuma chako ndipo adzalanda zinthu zako za malonda. Adzagwetsa makoma ako ndi kuwononga nyumba zako zabwino. Adzaponya miyala yako, matabwa ako ndi dothi lako mʼnyanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzalanda cuma cako ndi kufunkha malonda ako, nadzagwetsa malinga ako ndi kupasula nyumba zako zofunika, nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi pfumbi lako, m'madzi.