Ezekiel 26:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mafumu onse akunyanja adzatsika pa mipando yao yaufumu. Mikanjo yao adzaiika pambali, ndipo adzavula zovala zao zopetapeta zija. Adzachita mantha nakhala pansi akunjenjemera kosalekeza, ndipo adzangoti pakamwa gwirire poona zimene zakugwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo akalonga onse a kunyanja adzatsika ku mipando yachifumu yao, nadzavula zovala zao zopikapika, nadzavala kunjenjemera, nadzakhala panthaka pansi, nadzanjenjemera mphindi zonse ndi kudabwa nawe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mafumu a mʼmbali mwa nyanja adzatsika pa mipando yawo yaufumu. Adzayika pambali mikanjo yawo ndi kuvala zovala zawo zamakaka. Adzachita mantha ndipo adzakhala pansi akunjenjemera kosalekeza. Adzathedwa nzeru poona zimene zakugwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo akalonga onse a kunyanja adzatsika ku mipando yacifumu yao, nadzabvula zobvala zao zopikapika, nadzabvala kunjenjemera, nadzakhala panthaka pansi, nadzanjenjemera mphindi zonse ndi kukudabwa.