Ezekiel 26:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo adzayamba kuimba nyimbo yokudandaulira. Adzati, “ ‘Mzinda wotchuka iwe, nkuchita kuwonongeka chotere! Unali wamphamvu pa nyanja, iweyo ndi anthu ako. Iweyo ndi anthu ako munkaopsa anthu a m'mbali mwa nyanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kunena nawe, Watayika bwanji, ndiwe pokhala pa anthu a panyanja, mudzi womveka, unalimbika panyanja, uwo ndi okhalamo, amene anakhalitsa kuopsa kwao pa onse okhala momwemo!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo adzayimba nyimbo yokudandaula ndipo adzati kwa iwe: “ ‘Nʼkuchita kuwonongeka chotere, iwe mzinda wotchuka, wodzaza ndi anthu a ku nyanja! Unali wamphamvu pa nyanja, iwe ndi nzika zako; unkaopseza anthu onse amene ankakhala kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kunena nawe, Watayika bwanji, ndiwe pakhala pa anthu a panyanja, mudzi womveka, unalimbika panyanja, uwo ndi okhalamo, amene anakhalitsa kuopsa kwao pa onse okhala momwemo!