Ezekiel 26:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Tiro adanyodola Yerusalemu kuti, ‘Ha! Uja adaali chipata choloŵerapo mitundu ya anthuyu, waonongeka. Zipata zake zatitsekukira ife tsopano. Tilemera, poti iye tsopano wasanduka bwinja.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Tiro ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Onyo, wathyoka uwu udali chipata cha mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Turo ananyogodola Yerusalemu kuti ‘Hii! Uja amene anali chipata choloweramo anthu a mitundu ina wawonongeka. Zitseko zake zatsekukira ife. Tidzalemera popeza wasanduka bwinja.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Turo ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Onyo, watyoka uwu udali cipata ca mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;