Ezekiel 26:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikukukana iwe Tiro. Ndipo ndidzakubweretsera anthu a mitundu yambiri kuti adzalimbane nawe, monga momwe mafunde am'nyanja amaŵindukira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndikutsutsa iwe, Tiro, ndidzakukweretsera amitundu, monga nyanja iutsa mafunde ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulangani, inu anthu a ku Turo. Ndidzakuyitanirani anthu a mitundu ina kuti adzakulangeni monga momwe mafunde amawombera pa Nyanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona ndikutsutsa iwe, Turo, ndidzakukweretsera amitundu, monga nyanja iutsa mafunde ace.