Ezekiel 26:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a m'midzi yake yakumtunda adzaphedwa pa nkhondo. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ana ake akazi okhala kumunda adzaphedwa ndi lupanga; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu okhala ku mtunda adzasakazidwa ndi lupanga. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ana ace akazi okhala kumunda adzaphedwa ndi lupanga; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.