Ezekiel 26:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a m'midzi yako yakumtunda adzaŵapha pa nkhondo. Adzakuzinga ndi zithando zankhondo, ndiponso ndi ziwundo zankhondo. Adzakukwezera zishango kuti alimbane nawe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana ako akazi adzawapha kumunda ndi lupanga; ndipo adzakumangira nsanja, ndi kukuundira mtumbira, ndi kukuimikira chikopa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu okhala ku mtunda adzawapha ndi lupanga. Adzapanga mitumbira yankhondo ndi kukukwezera zishango kuti alimbane nawe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana ako akazi adzawapha kumunda ndi lupanga; ndipo adzakumangira nsanja, ndi kukuundira mtumbira, ndi kukuimikira cikopa.