Ezekiel 27:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankhondo a ku Arivadi ndi a ku Heleki ankalonda malinga ako ponse pozungulira. Anthu a ku Gamadi ankakwera pa nsanja zako, ndi kukapachika zishango zao pa malinga ako ponse pozungulira. Amenewo ndiwo amene ankakukongoletsa kwabasi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu a Arivadi pamodzi ndi ankhondo ako anali pa malinga ako pozungulira, ndi Agamadi anali mu nsanja zako; anapachika zikopa zao pa makoma ako pozungulira, anakwaniritsa kukoma kwako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Arivadi ndi Heleki ankalondera mbali zonse za mpanda wako; anthu a ku Gamadi anali mu nsanja zako, Iwo ankapachika zishango zawo pa makoma ako onse. Amenewo ndiwo anakukongoletsa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu a Ativadi pamodzi ndi ankhondo ako anali pa malinga ako pozungulira, ndi Agamadi anali mu nsanja zako; anapacika zikopa zao pa makoma ako pozungulira, anakwaniritsa kukoma kwako.