Ezekiel 27:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Dziko la Tarisisi linkachita nawe malonda chifukwa cha katundu wako wamtundumtundu, ndipo unkagulako siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu, mosinthana ndi katundu wako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tarisisi anagulana nawe malonda m'kuchuluka kwa chuma chilichonse; anagula malonda ako ndi siliva ndi chitsulo, seta ndi ntovu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Dziko la Tarisisi linachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako wamtundumtundu. Iwo ankapereka siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tarisi anagulana nawe malonda m'kucuruka kwa cuma ciri conse; anagula malonda ako ndi siliva ndi citsulo, seta ndi ntobvu.