Ezekiel 27:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Aramu ankagula zinthu zambiri zamalonda mosinthana ndi katundu wako wochuluka. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zofiirira, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korale ndi miyala ya rubi, mosinthana ndi katundu wako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aramu anachita nawe malonda chifukwa cha zambirizo udazipanga, anagula malonda ako ndi smaragido, nsalu yofiirira, ndi yopikapika, ndi bafuta, ndi korale, ndi ngale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu a ku Aramu ankachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zako. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zapepo, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korali ndi miyala ya rubi mosinthanitsa ndi katundu wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aramu anacita nawe malonda cifukwa ca zambirizo udazipanga, anagula malonda ako ndi smaragido, nsaru yofiirira, ndi yopikapika, ndi bafuta, ndi korale, ndi ngale.