Ezekiel 27:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yuda ndi Israele ankagula malonda ako. Iwo ankapereka tirigu, zipatso za olivi, nkhuyu zoyamba, ndiponso uchi, mafuta aolivi ndi zonunkhira zokometsera chakudya, mosinthana ndi katundu wako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yuda ndi dziko la Israele anagulana nawe malonda, anagula malonda ako ndi tirigu wa ku Miniti, ndi zozuna, ndi uchi, ndi mafuta, ndi mafuta amankhwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yuda ndi Israeli ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka tirigu ochokera ku Miniti ndi zokometsera zakudya, uchi, mafuta ndi mankhwala mosinthanitsa ndi katundu wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yuda ndi dziko la Israyeli anagulana nawe malonda, anagula malonda ako ndi tirigu wa ku Miniti, ndi zozuna, ndi uci, ndi mafuta, ndi mafuta amankhwala.