Ezekiel 27:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Damasiko ankagula kwa iwe chifukwa cha kuchuluka kwa zamalonda zako ndi katundu wako wosiyanasiyana. Ankakugulitsa vinyo wa ku Heliboni ndi ubweya wa nkhosa wambee.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Damasiko anagulana nawe malonda chifukwa cha zambirizo udazipanga, chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chilichonse, ndi vinyo wa ku Heliboni, ndi ubweya wa nkhosa woyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu a ku Damasiko, chifukwa cha zinthu zako za malonda zambiri ndi katundu wako wosiyanasiyana, ankachita nawe malonda a vinyo wochokera ku Heliboni ndi ubweya wankhosa ochokera ku Zahari.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Damasiko anagulana nawe malonda cifukwa ca zambirizo udazipanga, cifukwa ca kucuruka kwa cuma ciri conse, ndi vinyo wa ku Keliboni, ndi ubweya wa nkhosa woyera.