Ezekiel 27:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amalonda a ku Sheba ndi a ku Rama ankagulanso kwa iwe. Ankapereka zonunkhira zabwino kwambiri, miyala ya mtengo wapatali ndi golide yemwe, mosinthana ndi katundu wako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amalonda a ku Sheba ndi a ku Raama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa zilizonse, ndi miyala iliyonse ya mtengo wake, ndi golide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu amalonda a ku Seba ndi Raama ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka zonunkhira zosiyanasiyana zabwino kwambiri, miyala yokongola ndi golide mosinthanitsa ndi katundu wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amalonda a ku Seba ndi a ku Rama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa ziri zonse, ndi miyala iri yonse ya mtengo wace, ndi golidi.