Ezekiel 27:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu akumeneko ankasinthitsana nawe zovala zabwino kwambiri, nsalu zofiirira, nsalu zopetapeta, makalipeti amaŵangamaŵanga, zonsezo atazimanga bwino ndi zingwe zolimba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa anagulana nawe malonda ndi zovala zosankhika, ndi mitumba ya nsalu zofiirira ndi zopikapika, ndi chuma cha thonje lopotapota, ndi zingwe zopota zolimba za malonda ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwowa ankasinthanitsana nawe zovala zokongola, nsalu zopetapeta, zoyala pansi za mawangamawanga, atazimanga bwino ndi zingwe zolimba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa anagulana nawe malonda ndi zobvala zosankhika, ndi mitumba ya nsaru zofiirira ndi zopikapika, ndi cuma ca thonje lopotapota, ndi zingwe zopota zolimba za malonda ako.