Ezekiel 27:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zombo za ku Tarisisi zinkanyamula malonda ako. “Motero iweyo unali ngati chombo chapanyanja chodzaza ndi katundu wolemera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zombo za ku Tarisisi ndizo amtengatenga a malonda ako; ndipo unadzadzidwa ndi chuma ndi ulemu waukulu pakati pa nyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Sitima za pa madzi za ku Tarisisi zinali zonyamula malonda ako. Motero iwe uli ngati sitima yapamadzi yodzaza ndi katundu wolemera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zombo za ku Tarisi ndizo amtengatenga a malonda ako; ndipo unadzazidwa ndi cuma ndi ulemu waukuru pakati pa nyanja,