Ezekiel 27:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uuze Tiro, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, umene umachita malonda ndi anthu a mitundu yambiri ya ku maiko ambiri a m'mbali mwa nyanja, kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: “ ‘Iwe Tiro, wakhala ukunena kuti, “Ndine wokongola kwabasi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nuti kwa Tiro, Iwe wakukhala polowera m'nyanja, wakuchita malonda ndi mitundu ya anthu m'zisumbu zambiri, atero Ambuye Yehova, Iwe, Tiro, wati, Ine ndine wokongola wangwiro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uza Turo, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, wochita malonda ndi anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja kuti: Ambuye Yehova akuti, “Iwe Turo, umanena kuti, ‘Ndine wokongola kwambiri.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nuti kwa Turo, Iwe wakukhala polowera m'nyanja, wakucita malonda ndi mitundu ya anthu m'zisumbu zambiri, atero Ambuye Yehova, Iwe, Turo, wati, Ine ndine wokongola wangwiro.