Ezekiel 27:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akudzimeta mpala chifukwa cha iwe, ndipo akuvala ziguduli. Akulira ndi mitima yoŵaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nadzameta mpala chifukwa cha iwe, nadzadzimangira ziguduli m'chuuno, nadzakulirira ndi mtima wowawa maliro owawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akumeta mpala mitu yawo chifukwa cha iwe ndipo akuvala ziguduli. Akukulira iweyo ndi mitima yowawa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nadzameta mpala, cifukwa ca iwe, nadzadzimangira ziguduli m'cuuno, nadzakulirira ndi mtima wowawa maliro owawa.