Ezekiel 27:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Thanga lako linali la nsalu yabafuta. Nsalu yake inali yopeta bwino, yochokera ku Ejipito, ndipo ndiyo inali ngati mbendera yako. Nsalu zophimba mahema ako zinali zobiriŵira ndi zofiirira, zochokera ku zilumba za Elisa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Ejipito, likhale ngati mbendera yako; chophimba chako ndicho nsalu yamadzi ndi yofiirira zochokera ku zisumbu za Elisa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nsalu yabafuta yopeta yochokera ku Igupto inali thanga yako, ndipo inakhala ngati mbendera. Nsalu zophimba matenti ako zinali za mtundu wamtambo ndi pepo zochokera ku zilumba za Elisa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Aigupto, likhale ngati mbendera yako; cophimba cako ndico nsaru yamadzi ndi yofiirira zocokera ku zisumbu za Elisa.