Ezekiel 27:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa iwe munalinso akuluakulu ndi akatswiri a ku Gebala, amene ankakonza ziboo zako. Amalinyero ambiri m'zombo zao ankadzakuyendera kuchokera ku maiko onse kudzachita nawe malonda.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akulu a ku Gebala ndi eni luso ake anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amalinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu ndi eni luso a ku Gebala anali mʼkati mwako, ngati okonza zibowo zako. Sitima za pa nyanja zonse, ndi oyendetsa ake ankabwera pamodzi ndi katundu kudzachita nawe malonda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akr-ru a ku Gebala ndi eni luso ace anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amarinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda.