Ezekiel 28:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo ya maliro, kulira mfumu ya ku Tiro. Uiwuze mau angaŵa akuti, Udaali chitsanzo cha ungwiro weniweni. Udaali wanzeru ndiponso wokongola kwabasi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, kweza nyimbo ya maliro yolirira mfumu ya Tiro, nuziti kwa iye, Atero Ambuye Yehova, Wakomera muyeso ndi chizindikiro, wodzala ndi nzeru wokongola wangwiro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira mfumu ya Turo ndipo uyiwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti, “ ‘Iwe unali chitsanzo cha ungwiro weniweni, wodzaza ndi nzeru ndi wokongola kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, kweza nyimbo ya maliro yolirira mfumu ya Turo, nuziti kwa iye, Atero Ambuye Yehova, Wakomera muyeso ndi cizindikilo, wodzala ndi nzeru wokongola wangwiro.