Ezekiel 28:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Potanganidwa ndi zamalonda, udaachulukitsa zandeu ndi kumangochimwa. Nchifukwa chake ndidakuchotsa ku phiri langa lopatulika. Mngelo amene ankakulonda adakupirikitsa kuchokera ku miyala yamotoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa kuchuluka kwa malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi chiwawa, ndipo unachimwa; chifukwa chake ndinakukankha kukuchotsa pa phiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukuchotsa pakati pa miyala yamoto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Unatanganidwa ndi zamalonda. Zotsatira zake zinali zoti unachulukitsa zandewu ndi kumachimwa. Choncho ndinakuchotsa ku phiri langa lopatulika. Mkerubi amene ankakulondera uja anakupirikitsa kukuchotsa ku miyala yamoto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa kucuruka kwa malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi ciwawa, ndipo unacimwa; cifukwa cace ndinakukankha kukucotsa pa phiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukucotsa pakati pa miyala yamoto.