Ezekiel 28:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udachita zoipa zambiri pa kugula ndi kugulitsa zinthu, ndipo choncho malo ako achipembedzo udaŵaipitsa. Motero ndidabutsa moto pakati pako ndi kukupserezeratu. Onse okupenya tsopano amaona kuti ndiwe phulusa pa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa mphulupulu zako zochuluka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; chifukwa chake ndatulutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi malonda ako achinyengo unachulukitsa machimo ako. Motero unayipitsa malo ako achipembedzo. Choncho ndinabutsa moto pakati pako, ndipo unakupsereza, ndipo unasanduka phulusa pa dziko lapansi pamaso pa anthu onse amene amakuona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa mphulupulu zako zocuruka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; cifukwa cace ndaturutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona.