Ezekiel 28:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, uza mfumu ya ku Tiro mau angaŵa akuti, Iwe ndi mtima wako wodzikuza umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu. Ndimakhala ngati mfumu pa mpando wa milungu pakati pa nyanja yozama.’ Koma chonsecho ndiwe munthu chabe, osati mulungu, ngakhale umadziyesa wanzeru ngati mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Tiro, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine Mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, iwuze mfumu ya ku Turo mawu a Ine Ambuye Yehova akuti, “ ‘Iwe ndi mtima wako wodzikuza umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu; ndimakhala pa mpando wa mulungu pakati pa nyanja.’ Koma ndiwe munthu chabe osati mulungu, ngakhale ukuganiza kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Turo, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu,