Ezekiel 28:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine Ambuye Chauta ndikuti, ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni, ndipo anthu akadzaona zimene ndidzakuchite iwe, adzandilemekeza. Adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzakulanga ndipo ndikadzaonetsa pakati pako kuti Ine ndine woyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Sidoni, ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuchita Ine maweruzo mwa uwu, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa uwu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Ine Ambuye Yehova ndikuti, “ ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni, ndipo ndidzalemekezedwa chifukwa cha iwe. Anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova ndikadzakulanga ndi kudzionetsa kuti ndine woyera pakati pako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Zidoni, ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakucita Ine maweruzo mwa uwu, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa uwu.