Ezekiel 28:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakugwetsera mliri, ndipo m'miseu yako mudzayenderera mitsinje ya magazi. Anthu adzatha phu nkuphedwa, nkhondo idzakuzinga mbali zonse. Tsono anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndidzatumiza mliri ndi mwazi ilowe m'makwalala ake, ndi olasidwa adzagwa m'kati mwake ndi lupanga lougwera pozungulira ponse; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzatumiza mliri pa iwe ndi kuchititsa magazi kuti ayende mʼmisewu yako. Anthu ophedwa ndi lupanga adzagwa mbali zonse. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndidzatumiza mliri ndi mwazi ilowe m'makwalala ace, ndi olasidwa adzagwa m'kati mwace ndi lupanga lougwera pozungulira ponse; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.