Ezekiel 28:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nthaŵi imeneyo pafupi ndi Aisraele sipadzakhalanso anthu onyoza omaŵalasa ngati mitungwi, kapena omaŵapweteka ngati minga. Apo anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nyumba ya Israele siidzakhalanso nayo mitungwi yolasa, kapena minga yaululu ya aliyense wakuizinga ndi kuipeputsa; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Nthawi imeneyo Aisraeli sadzakhalanso ndi anthu pafupi achipongwe amene ali ngati nthula zowawa ndi ngati minga zopweteka. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nyumba ya Israyeli siidzakhalanso nayo mitungwi yolasa, kapena minga yaululu ya ali yense wakuizinga ndi kuipeputsa; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.