Ezekiel 28:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Nditasonkhanitsa Aisraele kuchokera ku mitundu ya anthu kumene adamwazikira, ndidzaonetsa kuyera kwanga mwa iwo, anthu a mitundu yonse akuwona. Aisraelewo adzakhalanso m'dziko lao limene ndidaapatsa mtumiki wanga Yakobe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, Pakusonkhanitsa nyumba ya Israele mwa mitundu ya anthu anabalalikamo, ndidzazindikirika Woyera mwaiwowa, pamaso pa amitundu; ndipo adzakhala m'dziko mwaomwao ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ine Ambuye Yehova mawu anga ndi awa: Nditasonkhanitsa Aisraeli kuchoka ku mayiko kumene anamwazikira, ndidzadzionetsa kuti ndine woyera pakati pawo pamaso pa anthu a mitundu ina. Adzakhala mʼdziko lawo, limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, Pakusonkhanitsa nyumba ya Israyeli mwa mitundu ya anthu anabalalikamo, ndidzazindikirika Woyera mwa iwowa, pamaso pa amitundu; ndipo adzakhala m'dziko mwao mwao ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga.