Ezekiel 28:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzakhala kumeneko mwamtendere, ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda yamphesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere, pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankaŵanyoza. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nadzakhalamo osatekeseka, nadzamanga nyumba, ndi kuoka mpesa m'mindamo, nadzakhalamo mosatekeseka, ndikatha kukwaniritsira maweruzo pa onse akuwapeputsa pozungulira pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzakhala kumeneko mwamtendere ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda ya mpesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankawanyoza. Motero iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nadzakhalamo osatekeseka, nadzamanga nyumba, ndi kunka mpesa m'mindamo, nadzakhalamo mosatekeseka, ndikatha kukwaniritsira maweruzo pa onse akuwapeputsa pozungulira pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao.