Ezekiel 28:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udachulukitsa chuma chako chifukwa cha nzeru zako zoyendetsera malonda, ndipo ukunyada chifukwa cha chuma chakocho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mwa nzeru zako zazikulu ndi kugulana malonda kwako wachulukitsa chuma chako, ndi mtima wako wadzikuza chifukwa cha chuma chako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi nzeru zako zochitira malonda unachulukitsa chuma chako ndipo wayamba kunyada chifukwa cha chuma chakocho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mwa nzeru zako zazikuru ndi kugulana malonda kwako wacurukitsa cuma cako, ndi mtima wako wadzikuza cifukwa ca cuma cako;