Ezekiel 28:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo kuti adzalimbane nawe. Iwowo ndi mtundu wa anthu ankhanza kwambiri. Adzakuthira nkhondo kuti aononge zokoma zonse zimene udazipata ndi nzeru zako, ndiponso kuti athyole kunyada kwako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake taona ndidzakufikitsira alendo oopsa a mitundu ya anthu, iwo adzasololera malupanga ao nzeru zako zokongola, nadzaipsa kunyezimira kwako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo, anthu ankhanza, kuti adzalimbane nawe. Adzakuthira nkhondo kuti awononge zonse zimene unazipeza ndi nzeru zako, ndipo adzawononga kunyada kwakoko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace taona, ndidzakufikitsira alendo oopsa a mitundu ya anthu, iwo adzasololera malupanga ao nzeru zako zokongola, nadzaipsa kunyezimira kwako.