Ezekiel 28:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi pamenepo udzanenabe kuti ndiwe mulungu pamaso pa anthu amene akukuphawo? Iyai, udzaoneka ngati munthu ndithu osati mulungu, pamene udzakhala m'manja mwa okuphawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi udzanenabe kuti, ‘Ine ndine mulungu,’ pamaso pa iwo amene akukupha? Iwe udzaoneka kuti ndiwe munthu chabe, osati mulungu, mʼmanja mwa iwo amene akukuphawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe.