Ezekiel 29:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ine ndikudana ndi iweyo, pamodzi ndi mitsinje yakoyo. Ndipo Ejipito ndidzamsandutsa bwinja, kuyambira ku mzinda wa Migidoli mpaka ku mzinda wa Siyene, kukafika ku malire a Etiopiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake taona, nditsutsana ndi iwe ndi mitsinje yako, ndipo ndidzasandutsa dziko la Ejipito likhale lopasuka konse, ndi labwinja, kuyambira ku Migidoli mpaka ku nsanja ya Siyene kufikira malire a Kusi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawe pamodzi ndi mitsinje yakoyo, ndipo ndidzasandutsa dziko la Igupto bwinja kuyambira chipululu cha Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani, kukafika ku malire a Kusi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace taona, nditsutsana ndi iwe ndi mitsinje yako, ndipo ndidzasandutsa dziko la Aigupto likhale lopasuka konse, ndi labwinja, kuyambira nsanja ya Sevene kufikira malire a Kusi.