Ezekiel 29:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko la Ejipito ndidzalisandutsa bwinja kupambana mabwinja a maiko ena onse. Pa zaka makumi anai mizinda yakenso idzakhala yopasuka kupambana mizinda ina yopasuka. Aejipitowo ndidzaŵamwaza pakati pa mitundu ya anthu, ndi kuŵabalalitsa pakati pa maiko ena.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzasandutsa dziko la Ejipito labwinja pakati pa maiko a mabwinja; ndi midzi yake pakati pa midzi yopasuka idzakhala yabwinja zaka makumi anai; ndipo ndidzamwaza Aejipito mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzasandutsa dziko la Igupto kukhala chipululu ngati zipululu za mayiko ena. Kwa zaka makumi anayi mizinda yakenso idzakhala yopasuka pakati pa mizinda yopasuka. Ndipo ndidzathamangitsira Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndi kuwabalalitsira mʼmayiko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzasandutsa dziko la Aigupto labwinja pakati pa maiko a mabwinja; ndi midzi yace pakati pa midzi yopasuka idzakhala yabwinja zaka makumi anai; ndipo ndidzamwaza Aaigupto mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.