Ezekiel 29:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ufumuwo udzasanduka wofooka kupambana maufumu ena onse, ndipo sudzadzikuzanso pakati pa mitundu ya anthu. Ndithudi Aejipito ndidzaŵachepetsa kwambiri, kotero kuti sadzatha kulamuliranso mitundu ina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzakhala wopepuka wa maufumu onse, sudzadzikwezanso pa amitundu; ndipo ndidzawachepsa, kuti asachitenso ufumu pa amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzakhala ufumu wotsika kwambiri kupambana maufumu ena onse ndipo sudzadzitukumula pakati pa mitundu ina. Ndidzawufowoketsa kwambiri kotero kuti sudzathanso kulamulira mitundu ya anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzakhala wopepuka wa maufumu onse, sudzadzikwezanso pa amitundu; ndipo ndidzawacepsa, kuti asacitenso ufumu pa amitundu.