Ezekiel 29:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele sadzadaliranso Ejipito. Ndipo chilango chimenechi chidzaŵakumbutsa kuchimwa kwao kuja pamene ankapempha Aejipito kuti aŵathandize. Motero Aisraele adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sudzakhalanso chotama cha nyumba ya Israele, kukumbutsa mphulupulu, pakuwatembenukira kuwatsata; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli sadzadaliranso Aigupto. Koma kuti chilango chawo chidzawakumbutsa tchimo lawo lija lofunafuna thandizo kuchokera ku Igupto. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sudzakhalanso cotama ca nyumba ya Israyeli, kukumbutsa mphulupulu, pakuwatembenukira kuwatsata; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.