Ezekiel 29:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, idaagwiritsa ntchito ankhondo ake pokathira nkhondo mzinda wa Tiro, mpaka munthu aliyense adachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo adanyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo, sadaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene adaigwirayo polimbana ndi mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anachititsa ankhondo ake ntchito yaikulu yoponyana ndi Tiro; mitu yonse inachita dazi, ndi mapewa onse ananyuka; koma analibe kulandira mphotho ya ku Tiro, iye kapena ankhondo ake, pa ntchito anagwirayo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara mfumu ya Babuloni inagwiritsa ntchito ankhondo ake kukathira nkhondo mzinda wa Turo, mpaka munthu aliyense anachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo ananyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo sanaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene anayigwira polimbana ndi mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anacititsa ankhondo ace nchito yaikuru yoponyana ndi Turo; mitu yonse inacita dazi, ndi mapewa onse ananyuka; koma analibe kulandira mphotho ya ku Turo, iye kapena ankhondo ace, pa nchito anagwirayo;