Ezekiel 29:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloniyo, ndidzampatsa Ejipito. Adzatenga chuma chake nadzachifunkha nkupita nacho. Zimenezi zidzakhala malipiro a gulu lake lankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzapereka dziko la Ejipito kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo adzachoka nao aunyinji ake, nadzafunkha ndi kulanda zake, ndizo mphotho ya khamu lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndidzapereka Igupto kwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, ndipo iyo idzatenga chuma chake ndi kuchifunkha ngati malipiro a gulu lake lankhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzapereka dziko la Aigupto kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo; ndipo adzacoka nao aunyinji ace, nadzafunkha ndi kulanda zace, ndizo mphotho ya khamu lace.