Ezekiel 29:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndampatsa dziko la Ejipito kuti akhale malipiro ake, chifukwa iye ndi ankhondo ake adandigwirira ntchito. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndamninkha dziko la Ejipito chombwezera ntchito yake, popeza anandigwirira ntchito, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndamupatsa Nebukadinezara Igupto ngati mphotho ya kulimbika kwake chifukwa iyo ndi gulu lake lankhondo anandigwirira ntchito, akutero Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndamninkha dziko la Aigupto combwezera nchito yace, popeza anandigwirira nchito, ati Ambuye Yehova.