Ezekiel 29:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ndidzakukola ndi mbedza m'kamwa mwako, nsomba za m'mitsinje mwako zidzakangamira ku mamba ako. Tsono ndidzakutulutsa mumtsinjemo pamodzi ndi nsomba zimene zakukangamira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndidzaika mbedza m'kamwa mwako, ndi kumamatiritsa nsomba za m'mitsinje mwako kumamba ako; ndipo ndidzakukweza kukutulutsa m'kati mwa mitsinje yako, pamodzi ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako zomamatira pa mamba ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako ndipo nsomba za mʼmitsinje yako zidzakangamira ku mamba ako. Tsono ndidzakutulutsa mu mtsinje mwakomo pamodzi ndi nsomba zimene zakangamira ku mamba ako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndidzaika mbedza m'kamwa mwako, ndi kumamatiritsa nsomba za m'mitsinje mwako ku mamba ako; ndipo ndidzakukweza kukuturutsa m'kati mwa mitsinje yako, pamodzi ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako zomamatira pa mamba ako.