Ezekiel 29:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakutaya ku chipululu, iweyo pamodzi ndi nsomba za m'mitsinje yako. Udzagwera ku thengo popanda wina wokutola kuti aike maliro ako. Ndidzakusandutsa chakudya cha zilombo ndi mbalame.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzakutaya kuchipululu, iwe ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako; udzagwa kuthengo koyera, sudzaunjikidwa, kapena kuoledwa; ndakupereka ukhale chakudya cha zilombo za padziko, ndi mbalame za kumlengalenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakutaya ku chipululu, iwe pamodzi ndi nsomba zonse za mʼmitsinje yako. Udzagwera pamtetete kuthengo popanda munthu woti akutole kuti akayike maliro ako. Ndidzakusandutsa chakudya cha zirombo za pa dziko lapansi ndi mbalame za mlengalenga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzakutaya kucipululu, iwe ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako; udzagwa kuthengo koyera, sudzaunjikidwa, kapena kuoledwa; ndakupereka ukhale cakudya ca zirombo za padziko, ndi mbalame za kumlengalenga,